28 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
29 Lankhula ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Wakubwera nayo nsembe yoyamika yace kwa Yehova, azidza naco copereka cace kwa Yehova cocokera ku nsembe yoyamika yace;
30 adze nazo m'manja mwace nsembe zamoto za Yehova; adze nao mafuta pamodzi ndi nganga, kuti aweyule ngangayo ikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.
31 Ndipo wansembeyo atenthe mafutawo pa guwa la nsembe; koma ngangayo ikhale ya Arent ndi ana ace.
32 Ndipo mwendo wathako wa ku dzanja lamanja muupereke kwa wansembe, ukhale nsembe yokweza yocokera ku nsembe zoyamika zanu.
33 Mwendo wathako wa ku dzanja lamanja ukhale gawo lace la iyeyu mwa ana a Aroni wakubwera Ilao mwazi wa zopereka zoyamika, ndi mafuta.
34 Pakuti ndatengako kwa ana a Israyeli, ku nsembe zoyamika zao, nganga ya nsembe yoweyula, ndi mwendo wathako wa ku dzanja lamanja wa nsembe yokweza; ndipo ndazipereka kwa Aroni wansembe ndi kwa ana ace, zikhale zoyenera iwo kosatha zocokera kwa ana a Israyeli.