10 Ndipo Yuda anamuka kwa Akanani akukhala m'Hebroni; koma kale dzina la Hebroni ndilo mudzi wa Ariba; ndipo anakantha Sesai, ndi Ahimani, ndi Talimai.
11 Pocoka pamenepo anamuka kwa nzika za ku Dibiri, koma kale dzina la Dibiri ndilo mudzi wa Seferi.
12 Ndipo Kalebe anati, iye amene akantha mudzi wa Seferi, naulanda, yemweyo ndidzampatsa Akisa mwana wanga wamkazi akhale mkazi wace.
13 Ndipo Otiniyeli, mwana wa Kenazi mng'ono wa Kalebi anaulanda, ndipo anampatsa Akisa mwana wace wamkazi akhale mkazi wace.
14 Ndipo kunali, m'mene anamdzera, anamkakamiza mwamuna wace kuti apemphe atate wace ampatse munda; natsika pa buru wace; ndipo Kalebe ananena naye, Ufunanji?
15 Ndipo anati kwa Iye, Mundipatse dalitso; popeza mwandipatsa dziko lakumwela, ndipatsenso zitsime za madzi. Pamenepo Kalebe anampatsa zitsime za kumtunda ndi zitsime za kunsi.
16 Ndipo ana a Mkeni mlamu wace wa Mose, anakwera kuturuka m'mudzi wa m'migwalangwa pamodzi ndi ana a Yuda, nalowa m'cipululu ca Yuda cokhala kumwela kwa Aradi; namuka iwo nakhala ndi anthuwo.