4 Ndipo Yuda atakwera, Yehova anapereka Akanani ndi Aperizi m'dzanja lao, ndipo anakantha a iwowa anthu zikwi khumi.
5 Ndipo anapeza Adoni-bezeki m'Bezeki, namthira nkhondo nakantha Akanani ndi Aperizi.
6 Koma Adoni-bezeki anathawa; ndipo anampitikitsa, namgwira, namdula zala zazikuru za m'manja ndi za m'mapazi.
7 Pamenepo anati Adoni-bezeki, Mafumu makumi asanu ndi awiri odulidwa zala zazikuru za m'manja ndi m'mapazi anaola kakudya kao pansi pa gome panga; monga ndinacita ine, momwemo Mulungu wandibwezera. Ndipo anadza naye ku Yerusalemu, nafa iye komweko.
8 Ndipo ana a Yuda anacita nkhondo pa Yerusalemu, naulanda, naukantha ndi lupanga lakuthwa, natentha mudzi ndi moto.
9 Ndipo atatero ana a Yuda anatsika kuthirana nao nkhondo Akanani akukhala kumapiri, ndi kumwela ndi kucidikha.
10 Ndipo Yuda anamuka kwa Akanani akukhala m'Hebroni; koma kale dzina la Hebroni ndilo mudzi wa Ariba; ndipo anakantha Sesai, ndi Ahimani, ndi Talimai.