12 nasiya Yehova Mulungu wa makolo ao, amene adawaturutsa m'dziko la Aigupto, natsata milungu yina, milungu ya mitundu ya anthu okhala pozungulira pao, naigwadira; nautsa mkwiyo wa Yehova.
13 Ndipo anasiya Yehova, natumikira Baala ndi Asitaroti.
14 Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Israyeli, ndipo anawapereka m'manja a ofunkha kuti awafunkhe; nawagulitsa m'dzanja la adani ao akuwazungulira osakhozanso iwowo kuima pamaso pa adani ao.
15 Kuli konse anaturuka, dzanja la Yehova linawakhalira moipa, monga Yehova adanena, ndi monga Yehova adawalumbirira; nasautsika kwambiri iwowa.
16 Ndipo Yehova anautsa oweruza, amene anawapulumutsa m'dzanja la iwo akuwafunkha.
17 Koma sanamvera angakhale oweruza ao, pakuti anamuka kupembedza milungu yina, naigwadira; anapambuka msanga m'njira yoyendamo makolo ao, pomvera malamulo a Yehova; sanatero iwowa.
18 Ndipo pamene Yehova anawaukitsira oweruza, Yehova anakhala naye woweruzayo, nawapulumutsa m'dzanja la adani ao masiku onse a woweruzayo; pakuti Yehova anagwidwa cisoni pa kubuula kwao cifukwa ca iwo akuwapsinja ndi kuwatsendereza.