15 Ndipo anawerenga ana a Benjamini a m'midzi tsiku lija amuna zikwi makumi awiri mphambu zisanu ndi cimodzi akusolola lupanga; osawerenga okhala m'Gibeya, ndiwo amuna osankhika mazana asanu ndi awiri.
16 Mwa anthu awa onse munali amuna osankhika mazana asanu ndi awiri amanzere, yense wa iwo amaponya mwala mwa maluli osaphonya.
17 Ndipo anawerenga amuna a Israyeli, osati Benjamini, amuna zikwi mazana anai osolola lupanga, anthu a nkhondo okha okha.
18 Nauka ana a Israyeli, nakwera kumka ku Beteli, nafunsira kwa Mulungu, nati, Ayambe ndani kutikwerera pa ana a Benjamini? Ndipo Yehova anati, Ayambe ndi Yuda.
19 Nauka ana a Israyeli m'mawa, naumangira Gibeya misasa.
20 Ndipo amuna a Israyeli anaturuka kulimbana ndi Benjamini; ndi amuna a Israyeli anawandandalikira nkhondo ku Gibeya.
21 Pamenepo ana a Benjamini anaturuka m'Gibeya, naononga a Israyeli tsiku lija zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, kuwagoneka pansi,