17 Ndipo anati kwa iye, Ngati mundikomera mtima mundionetse cizindikilo tsopano cakuti ndi Inu wakunena nane.
18 Musacoke pano, ndikupemphani, mpaka ndikudzerani ndi kuturutsa copereka canga ndi kuciika pamaso panu. Ndipo anati, Ndidzalinda mpaka ubwera.
19 Ndipo Gideoni analowa, nakonza kambuzi ndi mikate yopanda cotupitsa ya muyeso wa ufa; nyamayi anaiika m'licero, ndi msuzi anauthira mumbale, naturuka nazo kwa iye ali patsinde pa thundu, nazipereka.
20 Koma mthenga wa Mulungu ananena naye, Tenga nyamayi ndi mikate yopanda cotupitsa ndi kuziika pathanthwe pano ndi kutsanula msuzi. Ndipo anatero.
21 Pamenepo mthenga wa Yehova anatambasula nsonga ya ndodo inali m'dzanja lace, nakhudza nyamayi ndi mikate yopanda cotupitsa; ndipo unaturuka moto m'thanthwe nunyeketsa nyama ndi mikate yopanda cotupitsa; ndi mthenga wa Yehova anakanganuka pamaso pace.
22 Pamenepo Gideoni anaona kuti ndiye mthenga wa Yehova, nati Gideoni, Tsoka ine, Yehova Mulungu! popeza ndaona mthenga wa Yehova maso ndi maso.
23 Ndipo Yehova anati kwa iye, Mtendere ukhale ndi iwe, usaope, sudzafa.