20 Koma mthenga wa Mulungu ananena naye, Tenga nyamayi ndi mikate yopanda cotupitsa ndi kuziika pathanthwe pano ndi kutsanula msuzi. Ndipo anatero.
21 Pamenepo mthenga wa Yehova anatambasula nsonga ya ndodo inali m'dzanja lace, nakhudza nyamayi ndi mikate yopanda cotupitsa; ndipo unaturuka moto m'thanthwe nunyeketsa nyama ndi mikate yopanda cotupitsa; ndi mthenga wa Yehova anakanganuka pamaso pace.
22 Pamenepo Gideoni anaona kuti ndiye mthenga wa Yehova, nati Gideoni, Tsoka ine, Yehova Mulungu! popeza ndaona mthenga wa Yehova maso ndi maso.
23 Ndipo Yehova anati kwa iye, Mtendere ukhale ndi iwe, usaope, sudzafa.
24 Pamenepo Gideoni anammangira Yehova guwa la nsembe pomwepo; nalicha Yehova-ndiyemtendere; likali m'Ofira wa Abieziri ndi pano pomwe.
25 Ndipo kunali, usiku womwe uja Yehova ananena naye, Tenga ng'ombe ya atate wako, ndiyo ng'ombe yaciwiri ya zaka zisanu ndi ziwiri, nugamule guwa la nsembe la Baala ndilo la atate wako, nulikhe cifanizo ciri pomwepo;
26 numangire Yehova Mulungu wako guwa la nsembe pamwamba pa lingali, monga kuyenera; nutenge ng'ombe yaciwiriyo, nufukize nsembe yopsereza; nkhuni zace uyese cifanizo walikhaco.