13 Ndipo pakufikako Gideoni, taonani, panali munthu analikufotokozera mnzace loto, nati, Taona, kulota ndinalota, ndipo tapenya, mtanda wa mkate wabarele unakunkhulira-kunkhulira m'misasa ya Midyani, nufika kuhema, numgunda nagwa, numpidigula kuti hema anakhala cigwere.
14 Ndipo mnzace anayankha nati, Ici si cina konse koma lupanga la Gideoni mwana wa Yoasi, munthu wa Israyeli; Mulungu wapereka Midyani ndi a m'misasa onse m'dzanja lace.
15 Ndipo kunali, pakumva Gideoni kufotokozera kwa lotolo ndi tanthauzo lace, anadziwerama; nabwera ku misasa ya Israyeli nati, Taukani, pakuti Yehova wapereka a m'misasa a Midyani m'dzanja lanu.
16 Ndipo anagawa amuna mazana atatu akhale magulu atatu, napatsa malipenga m'manja a iwo onse, ndi mbiya zopanda kanthu, ndi miuni m'kati mwa mbiyazo,
17 Ndipo ananena nao, Mundipenyerere ine, ndi kucita momwemo; ndipo taonani, pakufika ine pa cilekezero ca misasa, kudzali, monga ndicita ine, momwemo muzicita inu.
18 Pamene ndiomba lipenga, ine ndi onse okhala nane, inunso muziomba lipenga pozungulira ponse pa misasa, ndi kunena kuti, Yehova ndi Gideoni.
19 Motero Gideoni ndi amuna zana anali naye anafikira ku cilekezero ca misasa poyambira ulonda wa pakati, atasintha alonda tsopano apa; ndipo anaomba malipenga, naphwanya mbiya zokhala m'manja mwao.