18 Pamene ndiomba lipenga, ine ndi onse okhala nane, inunso muziomba lipenga pozungulira ponse pa misasa, ndi kunena kuti, Yehova ndi Gideoni.
19 Motero Gideoni ndi amuna zana anali naye anafikira ku cilekezero ca misasa poyambira ulonda wa pakati, atasintha alonda tsopano apa; ndipo anaomba malipenga, naphwanya mbiya zokhala m'manja mwao.
20 Ndi magulu atatuwo anaomba malipenga, naswa mbiyazo, nagwira miuni ndi dzanja lao lamanzere, ndi malipenga m'dzanja lao lamanja kuwaomba; ndipo anapfuula, Lupanga la Yehova ndi la Gideoni.
21 Ndipo anaima yense m'mbuto mwace pozungulira misasa; pamenepo anathamanga a m'misasa onse, napfuula, nathawa.
22 Ndipo mazana atatuwa anaomba malipenga, ndipo Yehova anakanthanitsa yense mnzace ndi lupanga m'misasa monse; ndi a m'misasa anathawa mpaka ku Betesita ku Zerera, mpaka ku malire a Abelemehola pa Tabati.
23 Pamenepo anthu a Israyeli analalikidwa kucokera ku Nafitali, ndi ku Aseri, ndi ku Manase yense, nalondola Amidyani.
24 Gideoni anatumanso mithenga ku mapiri onse a Efraimu ndi kuti, Tsikani, kukomana ndi Amidyani ndi kutsekereza madooko asanafike iwowa, mpaka ku Beti-bara ndi Yordano. Potero amuna onse a Efraimu anasonkhana pamodzi natsekereza madooko mpaka ku Betibara, ndi Yordano.