15 Ndipo anafika kwa amuna a ku Sukoti, nati, Tapenyani Zeba ndi Tsalimuna amene munanditonza nao ndi kuti, Kodi manja a Zeba ndi Tsalimuna akhala m'dzanja lako, kuti tiwaninkhe mkate amuna ako akulema?
16 Ndipo anagwira akulu, a m'mudzi ndi minga ya kucipululu ndi mitungwi, nawalanga nazo amuna a ku Sukoti.
17 Ndipo anagamula nsanja ya Penueli, napha amuna a kumudzi.
18 Pamenepo anati kwa Zeba ndi Tsalimuna, Amunawo munawapha ku Tabori anali otani? Iwo nayankha, Monga iwe momwemo iwowa; yense wakunga mwana wa mfumu.
19 Ndipo anati, Ndiwo abale anga, ana a mai wanga. Pali Yehova mukadawasunga amoyo, sindikadakuphani.
20 Nati kwa Yeteri mwana wace woyamba, Tauka, nuwaphe. Koma mnyamatayo sanasolola lupanga lace; pakuti anaopa, pokhala anali mnyamata.
21 Pamenepo Zeba ndi Tsalimuna anati, Tauka iwe mwini nutigwere; pakuti monga munthu momwemo mphamvu yace. Ndipo Gideoni anauka nawapha Zeba ndi Tsalimuna, nalanda mphande zinali kukhosi kwa ngamila zao.