22 Pamenepo anthu a Israyeli anati kwa Gideoni, Mutilamulire ndi inu, ndi mwana wanu, ndi mdzukulu wanu, pakuti mwatipulumutsa m'dzanja la Amidyani.
23 Koma Gideoni ananena nao. Sindidzalamulira inu, ngakhale mwana wanga sadzalamulira inu; Yehova adzalamulira inu.
24 Gideoni anatinso kwa iwo, Mundilole ndipemphe kanthu kamodzi kwa inu, mundipatse ali yense mapelele mwa zofunkha zanu; pakuti anali nao mapelele agolidi, pokhala anali Aismayeli.
25 Ndipo anayankha, Kupereka tiwapereka; nayalapo cobvala, naponyamo yense mapelele a mwa zofunkha zao.
26 Ndipo kulemera kwace kwa mapelele agolidi adawapempha ndiko masekeli cikwi cimodzi ndi mazana asanu ndi awiri; osawerenga mphande, ndi zitunga ndi zobvala zacibakuwa za pa mafumu a ku Midyani, osawerenganso maunyolo okhala pa makosi a ngamila zao.
27 Ndipo Gideoni anawapanga fano, naliika m'mudzi mwace, ndiwo Ofira; ndi Israyeli yense analitsata kuligwadira pomwepo; ndipo linakhala kwa Gideoni ndi nyumba yace ngati msampha.
28 Motero anagonjetsa Amidyani pamaso pa ana a Israyeli, osaweramutsanso mitu yao iwowa. Ndipo dziko lidapumula zaka makumi anai m'masiku a Gideoni.