6 Koma akalonga a ku Sukoti anati, Kodi manja a Zeba ndi Tsalimuna ali m'dzanja lako tsopano apa, kuti ife tiwaninkhe ankhondo ako mkate?
7 Ndipo Gideoni anati, Cifukwa cace, Yehova akapereka Zeba ndi Tsalimuna m'dzanja langa, ndidzapuntha nyama yanu ndi minga ya m'cipululu ndi mitungwi.
8 Ndipo anacokapo kukwera ku Penueli, nanena nao momwemo; ndipo amuna a ku Penueli anamyankha monga adamyankha amuna a ku Sukoti.
9 Ndipo ananenanso kwa amuna a ku Penueli ndi kuti, Ndikabwerera ndi mtendere ndidzagumula nsanja iyi.
10 Zeba ndi Tsalimuna ndipo anali m'Karikori, ndi a m'misasa ao pamodzi nao, amuna monga zikwi khumi ndi zisanu; ndiwo otsala onse a khamu lonse la ana a kum'mawa; popeza atagwa amuna zikwi zana limodzi ndi makumi awiri akusolola lupanga.
11 Ndipo Gideoni anakwerera njira ya iwo okhala m'mahema kum'mawa kwa Noba, ndi Yogibea, nakantha khamulo popeza khamulo linakhala lokhazikika mtima.
12 Ndipo Zeba ndi Tsalimuna anathawa; koma anawatsata, nagwira mafumu awiri a Midyani Zeba ndi Tsalimuna, nanjenjemeretsa khamu lonse.