21 Pamenepo Yotamu anafulumira, nathawa, namuka ku Beeri, nakhala komweko, cifukwa ca Abimeleki mbale wace.
22 Abimeleki atakhala kalonga wa Israyeli zaka zitatu,
23 Mulungu anatumiza mzimu woipa pakati pa Abimeleki ndi eni ace a ku Sekemu; ndi eni ace a ku Sekemu anamcitira Abimeleki mosakhulupirika;
24 kuti ciwawa adacitira ana amuna makumi asanu ndi awiria Yerubaala cimdzere, ndi kuti mwazi wao uikidwe pa mbale wao Abimeleki anawaphayo, ndi pa eni ace a ku Sekemu, amene analimbikitsa manja ace, awaphe abale ace.
25 Ndipo eni ace a ku Sekemu anaika omlalira pamwamba pa mapiri; amene anawawanya onse akudzera njirayi; ndipo anamuuza Abimeleki.
26 Ndipo Gaala, mwana wa Ebedi anadza ndi abale ace, napita ku Sekemu; ndi eni ace a ku Sekemu anamkhulupirira.
27 Ndipo anaturuka kumka kuminda, nachera mphesa m'mindamo, naponda mphesa, napereka nsembe yolemekeza, nalowa m'nyumba ya mulungu wao, nadya, namwa, natemberera Abimeleki.