1 NDIPO atafa Mose mtumiki wa Yehova, Yehova anati kwa Yoswa mwana wa Nuni mnyamata wa Mose,
2 Mose mtumiki wanga wafa; tauka tsono, nuoloke Yordano uyu, iwe ndi anthu awa onse, kulowa m'dzikomo ndirikuwapatsa, ndiwo ana a Israyeli.
3 Pali ponse phazi lanu lidzapondapo ndinakupatsani, monga ndinanena ndi Mose.
4 Kuyambira cipululu, ndi Lebano uyu, kufikira mtsinje waukulu mtsinje wa Firate, dziko lonse la Ahiti, ndi kufikira nyanja yaikuru ku malowero a dzuwa, ndiwo malire anu.
5 Palibe munthu adzatha kuima pamaso pako masiku onse a moyo wako; monga ndinakhala ndi Mose momwemo ndidzakhala ndi iwe; sindidzakusowa, sindidzakusiya.
6 Khala wamphamvu, nulimbike mtima, pakuti udzagawira anthu awa dzikoli likhale colowa cao, ndilo limene ndinalumbirira makolo ao kuwapatsa.