9 Kodi sindinakulamulira iwe? Khala wamphamvu, nulimbike mtima, usaope, kapena kutenga nkhawa, pakuti Yehova Mulungu wako ali ndi iwe kuli konse umukako.
10 Pamenepo Yoswa analamulira akapitao a anthu, ndi kuti,
11 Pitani pakati pa cigono, nimulamulire anthu, ndi kuti, Mudzikonzeretu kamba, pakuti asanapite masiku atatu mudzaoloka Yordano uyu, kulowa ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, likhale lanu lanu.
12 Ndipo Yoswa anati kwa Arubeni, ndi Agadi, ndi pfuko la Manase logawika pakati, ndi kuti,
13 Kumbukilani mau amene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulirani inu, kuti, Yehova Mulungu wanu akupatsani mpumulo, nadzakupatsani dziko lino.
14 Akazi anu, ana anu, ndi zoweta zanu zikhale m'dzikoli anakuninkhani Mose, tsidya lino la Yordano; koma inu muoloke okonzeka kunkhondo pamaso pa abale anu, ngwazi zonse, ndi kuwathandiza;
15 mpaka Yehova atapatsa abale anu mpumulo, monga umo anakuninkhirani inu, naonso alandira dzikolo awaninkha Yehova Mulungu wanu; pamenepo mubwerere ku dziko lanu lanu, ndi kukhala nalo, limene Mose mtumiki wa Yehova anakupatsani tsidya lino la Yordano la kum'mawa,