3 kwa Akanani kwn'mawa ndi kumadzulo, ndi kwa Aamori ndi Ahiti, ndi Aperizi ndi Ayebusi kumapiri, ndi kwa Ahivi kunsi kwa Herimoni, m'dziko la Mizipa.
4 Ndipo anaturuka, iwo ndi makamu ao onse nao, anthu ambiri, kucuruka kwao ngati mcenga uli m'mphepete mwa nyanja; ndi akavalo ndi magareta ambirimbiri.
5 Ndipo mafwnu awa onse anasonkhana, nadza namanga pamodzi ku madzi a Meromu, kumthira Israyeli nkhondo.
6 Koma Yehova anati kwa Yoswa, Usaope cifukwa ca iwowa; pakuti mawa, dzuwa lino ndidzawapereka onse ophedwa pamaso pa Israyeli; uziwadula mitsindo akavalo ao, ndi kutentha agareta ao ndi moto.
7 Ndipo Yoswa, ndi anthu onse a nkhondo naye, anawadzera modzidzimutsa ku madzi a Meromu, nawagwera.
8 Ndipo Yehova anawapereka m'dzanja la Israyeli, ndipo anawakantha, nawapitikitsa mpaka ku Zidoni waukulu, ndi ku MiseripotuMaimu, ndi ku cigwa ca Mizepe kum'mawa; nawakantha mpaka sanawasiyira ndi mmodzi yense.
9 Ndipo Yoswa anawacitira monga Yehova adamuuza: nadula akavalo ao mitsindo, natentha magareta ao ndi moto.