1 Ndipo Yoswa anakalamba, wa zaka zambiri; ndipo Yehova ananena naye, Wakalamba, wa zaka zambiri, ndipo latsala dziko lalikurukuru, alilandire colowa cao,
2 Dziko lotsala ndilo: malire onse a Afilisti, ndi Agesuri onse,
3 kuyambira Sihoro wokhala cakuno ca Aigupto mpaka malire a Ekironu kumpoto, loyesedwa la Akanani; akalonga asanu a Afilisti, a ku Gaza, ndi a ku Asidodi, a ku Asekelo, a ku Giti, ndi a ku Ekiro, ndi Ahivi;
4 kumwela dziko lonse la Akanani, ndi Meara ndiwo wa Asidoni, mpaka ku Afeka, mpaka ku malire a Aaroori;
5 ndi dziko la Agebili, ndi Lebano lonse kum'mawa, kuyambira Baala-gadi pa tsinde la phiri la Herimoni, mpaka polowera pace pa Hamati;
6 nzika zonse za kumapiri kuyambira Lebano, mpaka Misirepotumaimu, Asidoni onse; ndidzawainga pamaso pa ana a Israyeli, koma limeneli uwagawire Aisrayeli, likhale colowa cao, monga ndinakulamulira.
7 Ndipo tsopano uwagawire mapfuko asanu ndi anai, ndi pfuko la Manase logawika pakati, dziko ili likhale colowa cao.