13 Koma Yoswa anampatsa Kalebe mwana wa Yefune gawo mwa ana a Yuda, monga Yehova adamlamulira, ndiwo mudzi wa Ariba, ndiye atate wa Anaki, ndiwo Hebroni.
14 Ndipo Kalebe anaingitsako ana amuna atatu a Anaki, ndiwo Sesai, ndi Ahimani, ndi Talimai, ana a Anaki.
15 Nakwera komweko kumka kwa nzika za Dibiri; koma kale dzina la Dibiri ndilo Kiriyati-Seferi.
16 Ndipo Kalebe anati, iye amene akantha Kiriyati-Seferi, naulanda, yemweyo ndidzampatsa Akisa mwana wanga akhale mkazi wace.
17 Ndipo Otiniyeli mwana wa Kenazi, mbale wace wa Kalebe, anaulanda; ndipo anampatsa Akisa mwana wace akhale mkazi wace.
18 Ndipo kunali, m'mene anamdzera, anamkangamiza mwamuna wace kuti apemphe atate wace ampatse munda; ndipo anatsika pa buru; pamenepo Kalebe ananena naye, Ufunanji?
19 Nati iye, Mundipatse dalitso; popeza mwandipatsa dziko la kumwela, ndipatseninso zitsime za madzi. Pamenepo anampatsa zitsime za kumtunda, ndi zitsime za kunsi.