4 Motero ana a Yosefe, Manase ndi Efraimu analandira colowa cao,
5 Ndipo malire a ana a Efraimu, monga mwa mabanja ao, ndiwo: malire a colowa cao kum'mawa ndiwo Atarotu-Adara, mpaka Betihoroni wa kumtunda;
6 naturuka malire kumadzulo ku Mikametatu kumpoto; nazungulira malire kum'mawa kumka ku Taanatu-silo, naupitirira kum'mawa kwace kwa Yanoa:
7 natsika kucokera ku Yanoa, kumka ku Atarotu, ndi ku Naara, nafika ku Yeriko, naturuka ku Yordano.
8 Kuyambira ku Tapua malire anamuka kumadzulo ku mtsinje wa Kana; ndi maturukiro ace anali kunyanja. Ici ndi colowa ca pfuko la ana a Efraimu monga mwa mabanja ao;
9 pamodzi ndi midzi adaipatulira ana a Efraimu pakati pa colowa ca ana a Manase, midzi yonse pamodzi ndi miraga yao.
10 Ndipo a sanaingitsa Akanani akukhala m'Gezeri; koma Akanani anakhala pakati pa Efraimu, kufikira lero lino, nawasonkhera msonkho.