9 M'gawo la ana a Yuda muli colowa ca ana a Simeoni; popeza gawo la ana a Yuda linawacurukira; cifukwa cace ana a Simeoni anali naco colowa pakati pa colowa coo.
10 Ndipo maere acitatu anakwecera ana a Zebuloni monga mwa mabanja ao; ndi malire a colowa cao anafikira ku Saridi;
11 nakwera malire ao kumka kumadzulo ndi ku Marala nafikira ku Dabeseti, nafikira ku mtsinje wa patsogolo pa Yokineamu;
12 ndi kucokera ku Saridi anazungulira kumka kum'mawa kumaturukira dzuwa, mpaka malire a Kisilotu-tabori; naturuka kumka ku Daberati, nakwera ku Yafia;
13 ndi pocoka pamenepo anapitirira kumka kum'mawa ku Gati-heferi, ku Etikazini; naturuka ku Remoni umene ulembedwa mpaka ku Nea,
14 nauzungulira malire kumpoto, kumka ku Hanatoni; ndi maturukiro ace anali ku cigwa ca Ifita-eli;
15 ndi Kata, ndi Nahalala ndi Simironi, ndi Idala ndi Betelehemu: midzi khumi ndi iwiri ndi miraga yao.