2 Ndipo wina anaiuza mfumu ya Yeriko, kuti, Taonani, usiku uno alowa muno amuna a ana a Israyeli, kulizonda dziko.
3 Ndipo mfumu ya Yeriko inatuma wina kwa Rahabi, ndi kuti, Turutsa amunawo anafika kwanu, amene analowa m'nyumba mwako; popeza anadzera kulizonda dziko lonse.
4 Koma mkaziyo anatenga amuna awiriwo, nawabisa; natero, Inde, amunawo anandifikira; koma sindinadziwa uko afuma;
5 ndipo m'mene akadati atseke pacipata, kutada, anaturuka amunawo; uko anamuka amunawo osakudziwa ine; muwalondole msanga, pakuti mudzawapeza.
6 Koma adawakweretsa patsindwi, nawabisa ndi mitengo yanthamza yoyanika patsindwi.
7 Ndipo amunawo anawalondola pa njira ya ku Yordano yomka kudooko; ndipo ataturuka akuwalondola, anatseka pacipata.
8 Koma asanagone iwo, anawakwerera patsindwi iye,