5 Ndipo akamlondola wolipsa mwazi, asampereke m'dzanja lace wakupha mnzaceyo; pakuti anakantha mnansi wace mosadziwa, osamuda kale.
6 Ndipo azikhala m'mudzimo mpaka adzaima pamaso pa msonkhano anene mlandu wace, mpaka atafa mkulu wansembe wa m'masiku omwewo; pamenepo wakupha mnzace azibwerera ndi kufika kumudzi kwace, ndi nyumba yace, kumudzi kumene adathawako.
7 Ndipo anapatula Kedesi m'Galileya ku mapiri a Nafitali, ndi Sekemu ku mapiri a Efraimu, ndi mudzi wa Ariba ndiwo Hebroni ku mapiri a Yuda.
8 Ndipo tsidya lija la Yordano kum'mawa kwa Yeriko, anaika Bezeri m'cipululu, kucidikha, wa pfuko la Rubeni, ndi Ramoti m'Gileadi wa ofuko la Gadi, ndi Golani m'Basana wa pfuko la Manase.
9 Iyi ndi midzi yoikidwira ana onse a Israyeli, ndi mlendo wakukhala pakati pao, kuti athawireko ali yense wakupha munthu, ndi kuti asafe ndi dzanja la wolipsa mwazi, asanaime pamaso pa msonkhano.