36 Ndipo motapira pa pfuko la Rubeni, Bezeri ndi mabusa ace, ndi Yahazi ndi mabusa ace,
37 Kedimotu ndi mabusa ace, ndi Mefati ndi mabusa ace; midzi inai.
38 Ndipo motapira m'pfuko la Gadi, Ramoti m'Gileadi ndi mabusa ace ndiwo mudzi wopulumukirako wakupha mnzaceyo, ndi Mahanaimu ndi mabusa ace;
39 Hesiboni ndi mabusa ace. Yazeri ndi mabusa ace: yonse pamodzi midzi inai.
40 Yonseyi ndiyo midzi ya ana a Merari monga mwa mabanja ao, ndiwo otsala a mabanja a Alevi; ndipo gawo lao ndilo midzi khumi ndi iwiri.
41 Midzi yonse ya Alevi, pakati pa colowa ca ana a Israyeli ndiyo midzi makumi anai kudza isanu ndi itatu, ndi mabusa ao.
42 Midzi iyi yonse inali nao mabusa ao pozungulira pao: inatero midzi iyi yonse.