21 Pamenepo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi pfuko la Manase logawika pakati anayankha, nanena ndi akuru a mabanja a Israyeli,
22 Yehova Cauta Mulungu, Yehova Cauta Mulungu, iye adziwa, ndi Israyeli adzadziwa; ngati mopikisana, ngati molakwira Yehova,
23 tadzimangira guwa la nsembe, kubwerera kusamtsata Yehova, musatipulumutsa lero lino; kapena ngati kufukizapo nsembe yopsereza, kapena nsembe yaufa, kapena kuperekapo nsembe zoyamika, acifunse Yehova mwini wace;
24 ndipo ngati ife sitinacita ici cifukwa ca kuopa mlandu, ndi kuti, Masiku akudzawo ana anu akadzanena ndi ana athu, ndi kuti, Muli ciani inu kwa Yehova Mulungu wa Israyeli?
25 pakuti Yehova anaika Yordano ukhale malire pakati pa ife ndi inu, ana a Rubeni, ndi ana a Gadi; mulibe gawo ndi Yehova; motero ana anu adzaleketsa ana athu asaope. Yehova.
26 Cifukwa cace tinati, Tiyeni tikonzeretu zotimangira guwa la nsembe, si kufukizapo nsembe yopsereza ai, kapena nsembe yophera ai;
27 koma lidzakhala mboni pakati pa ife ndi inu; ndi pakati pa mibadwo yathu ya m'tsogolo, kuti tikacita nchito ya Yehova pamaso pace ndi nsembe zathu zopsereza, ndi zophera, ndi zoyamika; kuti ana anu asanene ndi ana athu m'tsogolomo, Mulibe gawo ndi Yehova.