1 Ndipo atapita masiku ambiri, Yehova atapumulitsa Israyeli kwa adani ao onse akuwazungulira, ndipo Yoswa adakalamba nakhala wa zaka zambiri;
2 Yoswa anaitana Aisrayeli onse, akulu akulu ao, ndi akuru ao, ndi oweruza ao, ndi akapitao ao, nanena nao, Ndakalamba, ndine wa zaka zambiri;
3 ndipo munapenya zonse Yehova Mulungu anacitira mitundu iyi yonse ya anthu cifukwa ca inu; pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye anakuthirirani nkhondo.
4 Taonani, ndakugawirani mitundu ya anthu iyi yotsala ikhale colowa ca mapfuko anu, kuyambira ku Yordano, ndi mitundu yonse ya anthu ndinaipasula, mpaka ku nyanja yaikuru ku malowero a dzuwa.
5 Ndipo Yehova Mulungu wanu Iyeyu adzawapitikitsa pamaso panu, ndi kulanda dziko lao kuwacotsa pamaso panu, ndipo mudzalandira dziko lao likhale colowa canu; monga Yehova Mulungu wanu ananena ndi inu.