1 Ndipo Yoswa analawirira mamawa, kucoka ku Sitimu, nafika ku Yordano, iye ndi ana onse a Israyeli; nagona komweko, asanaoloke.
2 Ndipo kunali atapita masiku atatu, akapitao anapita pakati pa cigono;
3 nalamulira anthu, ndi kuti, Mukadzaona likasa la cipangano la Yehova Mulungu wanu, ndi ansembe Aleviwo atalisenza, pamenepo mucoke kwanu ndi kulitsata.
4 Koma pakhale dera pakati pa inu ndi ilo, monga mikono zikwi ziwiri poliyesa; musaliyandikire, kuti mudziwe njira imene muziyendamo; popeza simunapita njirayi kufikira lero.
5 Ndipo Yoswa ananena kwa anthu, Mudzipatule, pakuti mawa Yehova adzacita zodabwiza pakati pa inu.