5 Ndipo Yoswa ananena kwa anthu, Mudzipatule, pakuti mawa Yehova adzacita zodabwiza pakati pa inu.
6 Ndipo Yoswa anati kwa ansembe, Senzani likasa la cipangano, nimuoloke pamaso pa anthu. Nasenza iwo likasa la cipangano, natsogolera anthu.
7 Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, Lero lino ndidzayamba kukukuza pamaso pa Aisrayeli onse, kuti adziwe, kuti monga momwe ndinakhalira ndi Mose, momwemo ndidzakhala ndi iwe.
8 Ndipo uzilamulira ansembe akunyamula likasa la cipangano, ndi kuti, Pamene mufika kumphepete kwa madzi a Yordano muziima m'Yordano.
9 Ndipo Yoswa anati kwa ana a Israyeli, Idzani kuno, mumve mau a Yehova Molungu wanu.
10 Nati Yoswa, Ndi ici mudzadziwa kuti Mulungu wamoyo ali pakati pa inu, ndi kuti adzapitikitsa ndithu pamaso panu Akanani, ndi Ahiti, ndi Ahivi, ndi Aperizi, ndi Agirigasi, ndi Aamori, ndi Ayebusi.
11 Taonani, likasa la cipangano La Ambuye wa dziko lonse lapansi lioloka Yordano pamaso panu,