13 Tauka, patula anthu, nuti, Mudzipatulire mawa; pakuti atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Pali coperekedwa cionongeke pakati pako, Israyeli iwe; sukhoza kuima pamaso pa adani ako, mpaka mutacotsa coperekedwaco pakati panu.
14 Koma m'mawa adzakuyandikitsani, pfuko ndi pfuko; ndipo kudzali kuti pfukoli Yehova aliulula lidzayandikira mwa zibale zace; ndi cibale Yehova aciulula cidzayandikira monga mwa a nyumba ace; ndi a m'nyumbawo Yehova awaulula adzayandikira mmodzi mmodzi.
15 Ndipo kudzali kuti iye wogwidwa ali naco coperekedwaco adzatenthedwa ndi moto, iye ndi zonse ali nazo cifukwa analakwira cipangano ca Yehova, ndi cifukwa anacita copusa m'Israyeli.
16 Ndipo Yoswa analawira mamawa, nayandikizitsa Israyeli, pfuko ndi pfuko; ndi pfuko la Yuda linagwidwa;
17 nayandikizitsa zibale za Yuda, nagwira cibale ca Azari; nayandikizitsa cibale ca Azari, mmodzi mmodzi, nagwidwa Zabidi;
18 nayandikizitsa a m'nyumba yace mmodzi mmodzi; ndipo Akani, mwana wa Karimu, mwanu wa Zabidi, mwana wa Zera, wa pfuko la Yuda anagwidwa.
19 Ndipo Yoswa anati kwa Akani, Mwana wanga, ucitiretu ulemu Yehova Mulungu wa Israyeli, numlemekeze iye; nundiuze tsopano, wacitanji? usandibisire.