32 Ndipo mfumu Davide anati, Kandiitanireni Zadoki wansembeyo, ndi Natani mneneriyo, ndi Benaya mwana wa Yehoyada. Iwo nalowa pamaso pa mfumu.
33 Ndipo mfumu inati kwa iwo, Tengani akapolo a mfumu yanu, nimukweze Solomo mwana wanga pa nyuru yanga yanga, nimutsikire naye ku Gihoni.
34 Ndipo Zadoki wansembe ndi Natani mneneri akamdzoze kumeneko akhale mfumu ya Israyeli; ndipo muombe lipenga, ndi kuti, Mfumu Solomo akhale ndi moyo.
35 Pamenepo mumtsate iye, iye nadzadza nadzakhala pa mpando wanga wacifumu, popeza adzakhala iyeyu mfumu m'malo mwanga; ndipo ndamuika iye akhale mtsogoleri wa lsrayeli ndi Yuda.
36 Ndipo Benaya mwana wa Yehoyada anayankha mfumu, nati, Amen, ateronso Yehova Mulungu wa mbuye wanga mfumu.
37 Monga umo Yehova anakhalira ndi mbuye wanga mfumu, momwemo akhalenso ndi Solomo, nakuze mpando wace wacifumu upose mpando wacifumu wa mbuye wanga mfumu Davide.
38 Pamenepo Zadoki wansembe, ndi Natani mneneri, ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndi Akereti, ndi Apeleti aja anatsika, nakweza Solomo pa nyuru ya mfumu Davide, nafika naye ku Gihoni.