9 Ndipo Adoniya anapha nkhosa ndi ng'ombe ndi nyama zonona pamwala pa Zoheleti, uli pafupi ndi citsime ca Rogeli, naitana abale ace onse ana a mfumu, ndi anthu onse a Yuda anayamata a mfumu;
10 koma Natani mneneriyo, ndi Benaya, ndi anthu amphamvu aja, ndi Solomo mbale wace, sanawaitana.
11 Pamenepo Natani ananena ndi Batiseba amace wa Solomo, nati, Kodi sunamva kuti Adoniya mwana wa Hagiti walowa ufumu, ndipo Davide mbuye wathu sadziwa?
12 Ubwere tsono, ndikupangire, kuti usunge moyo wako, ndi moyo wa mwana wako Solomo.
13 Muka nulowe kwa mfumu Davide, nukati kwa iye, Mbuye wanga mfumu, kodi simunalumbirira mdzakazi wanu, ndi kuti, Zedi Solomo mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wadfumu? ndipo Adoniya akhaliranji mfumu?
14 Taona, uli cilankhulire ndi mfumu, inenso ndidzalowa pambuyo pako, ndi kutsimikiza mau ako.
15 Pamenepo Batiseba analowa kwa mfumu kucipinda; ndipo mfumuyo inali yokalamba ndithu; ndipo Abisagi wa ku Sunamu anali kutumikira mfumu.