1 Ndipo onani, munthu wa Mulungu anacokera ku Yuda mwa mau a Yehova nadza ku Beteli; ndipo Yerobiamu anali kuimirira m'mbali mwa guwa la nsembe kufukiza zonunkhira.
2 Ndipo iye anapfuula mwa mau a Yehova kutemberera guwa la nsembe, nati, Guwa la nsembe, guwa la nsembe, atero Yehova, Taona mwana adzabadwa m'nyumba ya Davide, dzina lace ndi Yosiya, adzaphera pa iwe ngati nsembe anthu ansembe a misanje, amene alikufukiza zonunkhira pa iwe, nadzatentha pa iwe mafupa a anthu.
3 Ndipo iye anapatsa cizindikilo tsiku lomwelo, nari, Cizindikilo cimene Yehova ananena ndi ici, Taonani guwali la nsembe lidzang'ambika, ndi phulusa liri pa ilo lidzatayika.
4 Ndipo kunacitika, pa kumva mfumu mau a munthu wa Mulungu amene anawapfuula, kutemberera guwa la nsembe m'Beteli, Yerobiamu anatansa dzanja lace ali ku guwalo, nati, Mgwireni iye. Ndipo dzanja lace analitansira kwa iye linauma, kuti sanatha kulipfunyatitsanso.