17 pakuti mau a Yehova anadza kwa ine, nati Usakadye mkate, kapena kumwa madzi kumeneko, kapena kubwerera njira yomweyo unadzerayo.
18 Ndipo anati kwa iye, Inenso ndine mneneri wonga iwe, ndipo mthenga analankhula ndi ine mwa mau a Yehova, nati, Kambwezere kwanu, kuti akadye mkate, namwe madzi. Koma anamnamiza.
19 Tsono anabwerera naye, nakadya kwao, namwa madzi.
20 Ndipo kunacitika iwo ali cikhalire pagome, mau a Yehova anadza kwa mneneri amene anambwezayo,
21 napfuula iye kwa munthu uja wa Mulungu anacokera ku Yudayo, nati, Atero Yehova, Pokhala sunamvera mau a pakamwa pa Yehova, osasunga lamulo lija Yehova Mulungu wako anakulamulira,
22 koma unabwerera nudya mkate, ndi kumwa madzi paja pomwe iye anakuuza, Usakadye mkate, kapena kumwa madzi, mtembo wako tsono sudzaikidwa ku manda a atate ako.
23 Ndipo kunacitika, atadya iye mkate, ndi kumwa madzi, anammangira mbereko pa buru mneneri amene anambwezayo.