12 Tanyamuka tsono, numuke kwanu; pakulowa mapazi ako m'mudzi mwanayo adzatsirizika.
13 Ndipo Aisrayeli onse adzamlira, nadzamuika, popeza iye yekha wa ana a Yerobiamu adzalowa m'manda; pakuti mwa iye mwapezedwa cokoma ca kwa Yehova Mulungu wa Israyeli m'nyumba ya Yerobiamu.
14 Ndiponso Yehova adzadziukitsira mfumu ya Israyeli, idzaononga nyumba ya Yerobiamu tsiku lomwelo; nciani ngakhale tsopano apa?
15 Popeza Yehova adzawakantha Aisrayeli monga bango ligwedezeka ndi madzi, nadzazula Aisrayeli m'dziko lino labwino analipatsa makolo ao, nadzawamwazira ku tsidya lija la Firate, popeza iwo anapanga zifanizo zao zokwiyitsa Yehova.
16 Ndipo adzai pereka Aisrayeli cifukwa ca macimo a Yerobiamu anacimwawo, nacimwitsa nao Aisrayeli.
17 Ndipo mkazi wa Yerobiamu ananyamuka nacoka, nafika ku Tiriza; ndipo polowa iye pa khomo la nyumba yace anatsirizika mwanayo.
18 Ndipo anamuika, namlira Aisrayeli, monga mwa mau a Yehova anawalankhula pa dzanja la mtumiki wace Ahiya mneneri.