2 Ndipo Eliya anamka kukadzionetsa kwa Ahabu. Ndipo njala inali yaikuru m'Samaria.
3 Ndipo Ahabu anaitana Obadiya woyang'anira nyumba yace. Koma Obadiya anaopa ndithu Yehova;
4 pakuti pamene Yezebeli anapulula aneneri a Yehova, Obadiya anatenga aneneri zana limodzi, nawabisa makumi asanu asanu m'phanga, nawadyetsa mkate ndi madzi.
5 Ndipo Ahabu anati kwa Obadiya, Kayendere dziko lonse ku zitsime zonse zamadzi, ndi ku mitsinje yonse, kapena tikapeza msipu ndi kusunga moyo wa akavalo ndi nyuru, zingafe nyama zonse.
6 Tsono iwo awiri anagawana dziko kukaliyendera; Ahabu anadzera njira yace yekha, ndi Obadiya njira yina yekha.
7 Ndipo Obadiya ali m'njira, taona, Eliya anakomana naye; iye namdziwa, namgwadira, nati, Ndinu kodi mbuye wanga Eliya?
8 Ndipo anamyankha, nati, Ndine amene; kauze mbuye wako kuti Eliya wabwera,