1 Ndipo Ahabu anauza Yezebeli zonse anazicita Eliya, ndi m'mene anawaphera ndi lupanga aneneri onsewo,
2 Tsono Yezebeli anatuma mthenga kwa Eliya, wakuti, Milungu indilange nionjezepo, ngati sindilinganiza moyo wako ndi moyo wa mmodzi wa iwowo mawa nthawi yomwe yino.
3 Ndipo iye ataona cimeneci, ananyamuka, nathawa kupulumutsa moyo, nafika ku Beereseba wa ku Yuda, nasiya mnyamata wace pamenepo.
4 Koma iye mwini analowa m'cipululu ulendo wa tsiku limodzi, nakakhala pansi patsinde pa mtengo watsanya, napempha kuti afe; nati, Kwafikira, cotsani tsopano moyo wanga, Yehova; popeza sindiri wokoma woposa makolo anga.
5 Ndipo anagona tulo patsinde pa mtengo watsanya; ndipo taonani, wamthenga anamkhudza, nati kwa iye, Uka nudye.