24 Tsono citani ici, cotsani mafumu aja yense ku malo ace, muike m'malo mwao akazembe.
25 Ndipo mudziwerengere khamu la nkhondo longa khamu lija lidaonongekalo, ndi akavalo onga akavalo aja, ndi magareta monga omwe aja; ndipo tikaponyane nao pacidikha tidzawapambana ndithu. Namvera iye mau ao, natero kumene.
26 Tsono kunacitika, pakufikanso caka Benihadadi anamemeza Aaramu nakwera ku Meld kukaponyana ndi Aisrayeli.
27 Ndipo Aisrayeli anamemezananso, anali naye kamba, nakakomana nao; ndipo Aisrayeli anamanga misasa yao pandunji pao, ngati timagulu tiwiri ta ana a mbuzi; koma Aaramu anadzaza dziko.
28 Ndipo munthu uja wa Mulungu anafikako, nalankhula ndi mfumu ya Israyeli, nati, Atero: Yehova, Popeza Aaramu amati, Yehova ndiye Mulungu wa kumapiri, osati Mulungu wa kuzigwa, mwa ici ndidzapereka unyinji uwu waukuru m'dzanja mwako, kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova.
29 Ndipo awa anakhala m'misasa pandunji pa ajawo masiku asanu ndi awiri. Tsono kunali, tsiku lacisanu ndi ciwiri anayambana nkhondo; ndipo ana a Israyeli anaphako Aaramu tsiku limodzi anthu oyenda pansi zikwi zana limodzi.
30 Ndipo otsalawo anathawira ku Afeki kumudzi, ndipo linga linawagwera anthu zikwi makumi awiri mphambu asanu ndi awiri amene adatsalawo. Ndipo Benihadadi anathawa, nalowa m'mudzi, m'cipinda ca m'katimo.