45 Tsono maciddwe ena a Yehosafati, ndi mphamvu anaionetsayo, ndi umo anathira nkhondo, kodi sizilembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda?
46 Ndipo anacotsa m'dziko anyamata onyansa aja adatsalira masiku a atate wace Asa.
47 Ndipo m'Edomu munalibe mfumu, koma kazembe wa mfumu.
48 Yehosafati anamanga zombo za ku Tarsisi kukatenga golidi ku Ofiri; koma sizinamuka, popeza zinaphwanyika pa Ezioni Geberi.
49 Pamenepo Ahaziyamwana wa Ahabu ananena ndi Yehosafati, Anyamata anga amuke pamodzi ndi anyamata anu m'zombo. Koma Yehosafati anakana.
50 Ndipo Yehosafati anagona ndi makolo ace, naikidwa ndi makolo ace m'mudzi wa Davide kholo lace; ndipo Yoramu mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.
51 Ahaziya mwana wa Ahabu anayamba kukhala mfumu ya Israyeli pa Samaria m'caka cakhumi mphambu zisanu ndi ziwiri ca Yehosafati mfumu ya Yuda; nakhala mfumu ya Israyeli zaka ziwiri.