25 Linasanjikika pa ng'ombe khumi mphambu ziwiri, zitatu zinapenya kumpoto, zitatu kumadzulo, zitatu kumwera, zitatu kum'mawa; ndipo thawalelo linakhazikika pamwamba pa izo; ndipo nkholo zao zinayang'anana.
26 Ndipo kucindikira kwace kunali ngati m'manja mwa munthu, ndipo mlomo wace unasadamuka ngati mlomo wa comwera, ngati maluwa akakombo, analowamo madzi a mitsuko yaikuru zikwi ziwiri.
27 Ndipo anapanga maphaka khumi amkuwa, m'litali mwace mwa phaka limodzi mikono inai, ndi kupingasa kwace mikono inai, ndi msinkhu wace mikono itatu.
28 Ndipo mapangidwe a maphakawo anali otere: anali nao matsekerezo ao, ndipo matsekerezo anali pakati pa mbano.
29 Ndipo pa matsekerezo a pakati pa mbano panali ngati mikango ndi ng'ombe ndi akerubi, ndi pamwamba pa mbano panali cosanjikirapo; ndipo pansi pa mikango ndi ng'ombe panaphatikizika zotsetseremba zoyangayanga zokoloweka.
30 Ndipo phaka lid lonse linali ndi njinga zamkuwa zinai ndi mitanda yamkuwa, ndipo ngondya zace zinai zinali ndi mapewa; pansi pa thawale panali mapewa oyengeka pa mbali pa zophatikizika zonse.
31 Ndipo pakamwa pace m'katimo pamwamba pa cosanjikira, panayesa mkono umodzi; koma pakamwa pace panali posadamuka, monga mapangidwe ace a cosanjikira, mkono umodzi ndi nusu; ndiponso pakamwa pace panali zolemba ndi matsekerezo ace anali amphwamphwa, si ozunguniza.