1 Pamenepo Solomo anasonkhanitsa akulu a Israyeli, ndi akulu onse a mafuko, akalonga a nyumba za atate a ana a Israyeli, kwa mfumu Solomo m'Yerusalemu, kukatenga likasa la cipangano ca Yehova m'mudzi wa Davide, ndiwo Ziyoni.
2 Ndipo anthu onse a Israyeli anasonkhana kwa mfumu Solomo kukadyereram'mwezi wa Etanimu, ndiwo mwezi wacisanu ndi ciwiri.
3 Ndipo akulu onse a Israyeli anadza, ansembe nanyamula likasa.
4 Ndipo anatenga likasa la Yehova, ndi cihema cokomanako, ndi zipangizo zonse zopatulika, zinali m'cihemamo, inde zimenezi anazitenga ansembe ndi Alevi.
5 Ndipo mfumu Solomo ndi msonkhano wonse wa Israyeli wosonkhana kwa iye anali naye kulikasa, naphera nkhosa ndi ng'ombe za nsembe zosawerengeka ndi zosadziwika, cifukwa ca unyinji wao.
6 Ndipo ansembe analonga likasa la cipangano ca Yehova kumalo kwace, ku monenera mwa nyumba, ku malo opatulikitsa, munsi mwa mapiko a akerubi,
7 Popeza akerubiwo anatambasula mapiko ao awiri pamwamba pa likasa, ndipo akerubiwo anaphimba pamwamba pa likasa ndi mphiko zace.