20 Ndipo Yehova wakhazikitsa mau ace analankhulawo, ndipo ndauka ndine m'malo mwa Davide atate wanga, ndipo ndikhala pa mpando wacifumu wa Israyeli monga adalonjeza Yehova, ndipo ndamangira dzina la Yehova Mulungu wa Israyeli nyumba.
21 Ndipo ndakonzera malo likasalo, m'mene muli cipangano ca Yehova, cimene anapangana ndi makolo athu pamene anawaturutsa m'dziko la Aigupto.
22 Ndipo Solomo anaimirira ku guwa la nsembe la Yehova pamaso pa msonkhano wonse wa Israyeli, natambasulira manja ace kumwamba, nati,
23 Yehova Mulungu wa Israyeli, palibe Mulungu wolingana ndi inu m'thambo la kumwamba, kapena pa dziko lapansi, wakusungira cipangano ndi cifundo akapolo anu akuyenda ndi mtima wonse pamaso panu,
24 wakusungira mtumild wanu Davide atate wanga cimene mudamlonjezaco; munalankhulanso m'kamwa mwanu ndi kukwaniritsa ndi dzanja lanu monga lero lino.
25 Ndipo tsopano, Yehova Mulungu wa Israyeli, msungireni mtumiki wanu Davide atate wanga cimene cija mudamlonjezaco, ndi kuti, Sadzakusowa munthu pamaso panga wokhala pa mpando wacifumu wa Israyeli; komatu ana ako acenjere njira yao, kuti akayende pamaso panga monga umo unayendera iwe pamaso panga.
26 Ndipo tsopano, Mulungu wa Israyeli, atsimikizike mau anu amene munalankhula ndi mtumiki wanu Davide atate wanga.