39 pamenepo mverani Inu m'Mwamba mokhala Inu, ndi kukhululukira, ndi kucita, ndi kubwezera munthu yense monga njira zace zonse, amene Inu mumdziwa mtima wace, popeza Inu, Inu nokha, mudziwa mitima ya ana onse a anthu;
40 kuti aope Inu masiku onse akukhala iwowo m'dziko limene Inu munapatsa makolo ao.
41 Ndiponso kunena za mlendo, wosati wa anthu anu Aisrayeli, koma wakufumira m'dziko lakutali cifukwa ca dzina lanu,
42 popeza adzamva za dzina lanu lalikuru ndi dzanja lanu lamphamvu ndi mkono wanu wotambasuka; akabwera iyeyo nadzapemphera molunjika ku nyumba yino;
43 mverani Inu m'Mwamba mokhala Inu, ndipo citani monga mwa zonse mlendoyo azipempha kwa Inu; kuti anthu onse a dziko lapansi adziwe dzina lanu, kuopa Inu, monga amatero anthu anu Aisrayeli, ndi kuti adziwe kuti nyumba yino ndaimangayi yachedwa dzina lanu.
44 Akaturuka anthu anu kukayambana nkhondo ndi adani ao, kumene konse inu mudzawatuma, ndipo akapemphera kwa Yehova molunjika ku mudzi uno munausankha Inu, ndi ku nyumba ndamangira dzina lanu;
45 pamenepo mverani Inu m'Mwamba pempho ndi pembedzero lao, ndi kulimbitsa mlandu wao.