59 Ndipo mau anga amenewa ndapembedzera nao pamaso pa Yehova akhale pafupi ndi Yehova Mulungu wathu usana ndi usiku, kuti alimbitse mlandu wa kapolo wace, ndi mlandu wa anthu ace Aisrayeli, mlandu wa tsiku pa tsiku lace;
60 kuti anthu onse a pa dziko lapansi akadziwe kuti Yehova ndiye Mulungu, palibe wina.
61 Mitima yanu ikhale yangwiro ndi Yehova Mulungu wathu, kuyenda m'malemba ace ndi kusunga malamulo ace, monga lero lino.
62 Ndipo mfumu ndi anthu onse a Israyeli pamodzi naye anaphera nsembe pamaso pa Yehova.
63 Ndipo Solomo anaphera nsembe yamtendere, yophera kwa Yehova ng'ombe zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, ndi nkhosa zikwi zana limodzi mphambu makumi awiri. Momwemo mfumu ndi ana a Israyeli onse anapereka nyumbayo ya Yehova.
64 Tsiku lomwelo mfumu inapatulira Mulungu pakati pace pa bwalo la ku khomo la nyumba ya Yehova; pakuti pomwepo anapereka nsembe yopsereza ndi nsembe yaufa, ndi mafuta a nsembe zamtendere; popeza guwa la nsembe lamkuwa linali pamaso pa Yehova lidacepa kulandira nsembe zopsereza, ndi nsembe zaufa, ndi mafuta a nsembe zamtendere.
65 Ndipo nthawi yomweyo Solomo anacita madyerero pamaso pa Yehova Mulungu wathu, ndi Israyeli yense pamodzi naye, msonkhano waukuru wakuyambira polowera ku Hamati kufikira ku nyanja ya ku Aigupto, masiku asanu ndi awiri, ndi masiku asanu ndi awiri ena, ndiwo masiku khumi mphambu anai.