6 Pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu amuphe iye amene akuti afe; asamuphe pakamwa pa mboni imodzi.
7 Liyambe kumgwera dzanja la mboniyo kumupha; pamenepo dzanja la anthu onse, Potero muzicotsa coipaco pakati panu.
8 Ukakulakani mlandu pouweruza, ndiwo wakunena zamwazi, kapena zakutsutsana, kapena zakupandana, ndiyo mirandu yakutengana m'midzi mwanu; pamenepo muziuka ndi kukwera kumka ku malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha;
9 nimufike kwa ansembe, Alevi, ndi kwa woweruza wa m'masiku awo; nimufunsire; ndipo adzakufotokozerani maweruzidwe ace.
10 Ndipo mucite monga momwe ananena mau akufotokozeraniwo, ku malo amene Yehova adzawasankha; nimusamalire kucita monga mwa zonse akulangizanizi,
11 Monga momwe anena malamulo akulangizani, ndi monga mwa ciweruzo akufotokozerani, mucite; mau akufotokozerani musawapatukire kulamanja kapena kulamanzere.
12 Koma munthu wakucita modzikuza, osamvera wansembe wokhala ciriri kutumikirako pamaso pa Yehova Mulungu wanu, kapena woweruza, munthuyo afe; ndipo mucotse coipaco kwa Israyeli.