15 Penyani muli mokhalamo mwanu mopatulika, m'mwamba, ndipo dalitseni anthu anu Israyeli, ndi nthaka imene munatipatsa, monga munalumbirira makolo athu, dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi.
16 Lero lino Yehova Mulungu wanu akulamulirani kucita malemba ndi maweruzo awa; potero muzimvera ndi kuwacita ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse.
17 Mwalonjezetsa Yehova lero kuti adzakhala Mulungu wanu, ndi kuti mudzayenda m'njira zace, ndi kusunga malemba ace, ndi malamulo ace, ndi maweruzo ace, ndi kumvera mau ace.
18 Ndipo Yehova wakulonjezetsani lero kuti mudzakhala anthu ace ace a pa okha, monga ananena ndi inu, ndi kuti mudzasunga malamulo ace onse;
19 kuti akukulitseni koposa amitundu onse anawalenga, wolemekezeka, womveka dzina, ndi waulemu; ndi kuti mukhale mtundu wa anthu wopatulikira Yehova Mulungu wanu monga ananena.