21 Ndipo Yehova adzamsiyanitsa ndi mafuko onse a Israyeli ndi kumcitira coipa, monga mwa matemberero onse a cipangano colembedwa m'buku ili la cilamulo.
22 Ndipo mbadwo ukudza, ana anu akuuka mutafa inu, ndi mlendo wocokera ku dziko lakutali, adzati, pakuona iwo miliri ya dziko ili, ndi nthendazi; Yehova awadwalitsa nazo,
23 ndi kuti lidapsa dziko lace lonse ndi sulfure, ndi mcere, kuti sabzalamo, kapena siliphukitsa kanthu kapena sumerapo msipu, monga kupasula kwace kwa Sodomu ndi Gomora, Adima, ndi Zeboimu, imene Yehova anaipasula m'mkwiyo wace ndi ukali wace;
24 inde amitundu onse adzati, Yehova anacitira dziko ili cotero cifukwa ninji? nciani kupsa mtima kwakukuru kumene?
25 Pamenepo adzati, Popeza analeka cipangano ca Yehova, Mulungu wa makolo ao, cimene anacita nao pakuwaturutsa m'dziko la Aigupto;
26 napita natumikira milungu yina, naigwadira, milungu imene sanaidziwa, imene sanawagawira;
27 cifukwa cace Mulungu anapsera mtima dziko ili kulitengera temberero lonse lolembedwa m'buku ili.