16 amene anakudyetsani m'cipululu ndi mana, amene makolo anu sanawadziwa; kuti akucepetseni, ndi kuti akuyeseni, kuti akucitireni cokoma potsiriza panu;
17 ndipo munganene m'mtima mwanu, Mphamvu yanga ndi mkono wanga wolimba zinandifunira cuma ici.
18 Koma mukumbukile Yehova Mulungu wanu, popeza ndi Iyeyu wakupatsani mphamvu yakuonera cuma; kuti akhazikitse cipangano cace cimene analumbirira makolo anu, monga cikhala lero lino.
19 Ndipo kudzakhala kuti mukaiwalatu Yehova Mulungu wanu, ndi kutsata milungu yina ndi kuitumikira, ndikucitirani mboni lero lino kuti mudzaonongeka ndithu.
20 Monga amitundu amene Yehova awaononga pamaso panu, momwemo mudzaonongeka; cifukwa ca kusamvera mau a Yehova Mulungu wanu.