1 Mose ndi Aroni, nati,
2 Nenani nao ana a Israyeli, nimuti nao, Pamene mwamuna ali yense ali ndi nthenda yakukha m'thupi mwace, akhale wodetsedwa, cifukwaca kukha kwace.
3 Ndipo kudetsedwa kwa kukha kwace ndiko: ngakhale cakukhaco cituruka m'thupi mwace, ngakhale caleka m'thupi mwace, ndiko kumdetsa kwace.
4 Kama ali yense agonapo wakukhayo ali wodetsedwa; ndi cinthu ciri conse acikhalira ciri codetsedwa.
5 Ndipo munthu ali yense wakukhudza kama wace azitsuka zobvala zace, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo,
6 Ndipo iye wakukhalira cinthu ciri conse adacikhalira wakukhayo atsuke zobvala zace, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.