25 Ndipo mkazi akakhala ndi kukha mwazi masiku ambiri, osati masiku a kuoloka kwace, kapena akamakha kupitirira nthawi ya kuoloka kwace; masiku onse cirinkukha comdetsa cace, adzakhala wodetsedwa, monga masiku a kuoloka kwace.
26 Kama ali yense agonapo masiku a kukha kwace akhale ngati kama wa kuoloka kwace; ndi cinthu ciri conse akhalapo ciri codetsedwa, ngati kudetsa kwa kuoloka kwace.
27 Ndipo munthu ali yense akakhudza zimenezi adzakhala wodetsedwa, natsuke zobvala zace, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
28 Koma akayeretsedwa kukha kwace, adziwerengere masiku asanu ndi awiri, ndipo atatero adzakhala woyeretsedwa.
29 Ndipo tsiku lacisanu ndi citatu atenge njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, nafike nazo kwa wansembe ku khomo la cihema cokomanako.
30 Ndipo wansembe apereke limodzi likhale nsembe yaucimo, ndi linalo likhale nsembe yopsereza; ndipo wansembe amcitire comtetezera pamaso pa Yehova cifukwa ca kukha kwace komdetsa.
31 Motero muzipatula ana a Israyeli kwa kudetsedwa kwao; angafe m'kudetsedwa kwao, pamene adetsa kacisi wanga ali pakati pao.