19 Ndipo awazepo mwazi wina ndi cala cace kasanu ndi katatu; ndi kuliyeretsa ndi kulipatula kulicotsera zodetsa za ana a Israyeli.
20 Ndipo atatha kucitira cotetezera malo opatulika, ndi cihema cokomanako, ndi guwa la nsembe, abwere nayo mbuzi yamoyo;
21 ndipo Aroni aike manja ace onse awiri pamutu pa mbuzi yamoyo, ndi kubvomereza pa iyo mphulupulu zonse za ana a Israyeli, ndi zolakwa zao zonse, monga mwa zocimwa zao zonse; naike izi pamutu pa mbuziyo, ndi kuitumiza kucipululu ndi dzanja la munthu wompangiratu,
22 ndi mbuziyo isenze yokha mphulupulu zonsezo kumka nazo ku dziko la pa lokha; ndipo azitaya mbuziyo m'cipululu.
23 Pamenepo Aroni alowe m'cihema cokomanako, nabvule zobvala zabafuta zimene anazibvala polowa m'malo opatulika, nazisiye komweko.
24 Ndipo asambe thupi lace ndi madzi kumalo kopatulika, nabvale zobvala zace, naturuke, napereke nsembe yopsereza yace, ndi nsembe yopsereza ya anthu, nacite codzitetezera yekha ndi anthu.
25 Ndipo atenthe mafuta a nsembe yaucimo pa guwa la nsembe.