20 Usagona naye mkazi wa mnansi wako, kudetsedwa naye limodzi.
21 Ndipo usamapereka a mbumba yako kuwapitiriza kumoto cifukwa ca Moleke, usamaipsa dzina la Mulungu wako: Ine ndine Yehova.
22 Usamagonana ndi mwamuna, monga amagonana ndi mkazi; conyansa ici.
23 Ndipo usamagonana ndi nyama iri yonse, kudetsedwa nayo; kapena mkazi asamaima panyama, kugonana nayo; cisokonezo coopsa ici.
24 Musamadzidetsa naco cimodzi ca izi; pakuti amitundu amene ndiwapitikitsa pamaso panu amadetsedwa nazo zonsezi;
25 dziko lomwe lidetsedwa; cifukwa cace ndililanga, ndi dzikoli lisanza okhala m'mwemo.
26 Koma inu, muzisunga malemba anga ndi maweruzo anga, osacita cimodzi conse ca zonyansa izi; ngakhale wa m'dziko ngakhale mlendo wakugonera pakati pa inu;